1 Samuel 11:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adauza amithenga a ku Yabesi aja kuti, “Mukaŵauze anthu akwanu kuti maŵa, dzuŵa likuwomba mtengo, adzapulumutsidwa.” Anthu a ku Yabesi atamva uthengawu, adasangalala zedi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa mithenga inadzayi, Muzitero kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, Mawa litatentha dzuwa, mudzaona chipulumutso. Ndipo mithenga inadza niuza a ku Yabesi; nakondwera iwowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Sauli anawuza amithenga ochokera ku Yabesi aja kuti, “Mukawawuze anthu a ku Yabesi Giliyadi kuti mawa nthawi ya masana adzapulumutsidwa.” Pamene amithengawo anapita ndi kukafotokoza nkhani imeneyi kwa anthu a ku Yabesi, iwo anasangalala kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa mithenga inadzayi, Muzitero kwa anthu a ku Yabezi Gileadi, Mawa litatentha dzuwa, mudzaona cipulumutso. Ndipo mithenga inadza niuza a ku Yabezi; nakondwara iwowa.