1 Samuel 12:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iwowo adadandaula kwa Chauta nati. ‘Ife tachimwa chifukwa choti tasiya Inu Chauta, ndipo tatumikira mafano aja a Baala ndi Asitaroti. Koma tsopano tipulumutseni kwa adani athu, ndipo tidzakutumikirani.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapemphera kwa Yehova, kuti, Tinachimwa, popeza tinasiya Yehova, ndi kutumikira Abaala ndi Asitaroti, koma mutipulumutse tsopano m'manja a adani anthu, ndipo tidzakutumikirani Inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono iwo analira kwa Yehova nati, ‘Ife tachimwa, chifukwa tamusiya Yehova ndi kumatumikira mafano a Baala ndi Asiteroti. Koma tsopano tilanditseni mʼmanja mwa adani athu ndipo tidzakutumikirani.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapemphera kwa Yehova, kuti, Tinacimwa, popeza tinasiya Yehova, ndi kutumikira Abaala ndi Asitaroti, koma mutipulumutse tsopano m'manja a adani anthu, ndipo tidzakutumikirani Inu.