1 Samuel 12:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukamaopa Chauta ndi kumamtumikira ndi kumamvera mau ake, osakana malamulo ake, ndiponso ngati nonsenu pamodzi ndi mfumu yanu mudzatsata Chauta, Mulungu wanu, zonse zidzakuyenderani bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukaopa Yehova ndi kumtumikira ndi kumvera mau ake, ndi kusakana lamulo lake la Yehova, ndipo inu ndi mfumu imene iweruza inu mukadzatsata Yehova Mulungu wanu, chabwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati muziopa Yehova ndi kumamutumikira ndi kumamumvera, osamupandukira ndiponso ngati inu pamodzi ndi mfumu yanu mudzatsata Yehova Mulungu wanu, ndiye zinthu zonse zidzakuyenderani bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukaopa Yehova ndi kumtumikira ndi kumvera mau ace, ndi kusakana lamulo lace la Yehova, ndipo inu ndi mfumu imene iweruza inu mukadzatsata Yehova Mulungu wanu, cabwino.