1 Samuel 12:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ino si nthaŵi yachilimwe yodula tirigu? Komabe nditama Chauta mopemba kuti agwetse mvula yamabingu. Apo mudziŵa ndi kuwona kuti tchimo lanu limene mwachita popempha mfumu kwa Chauta nlalikulu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Si nyengo yakumweta tirigu lero kodi? Ndidzaitana kwa Yehova, kuti atumize bingu ndi mvula; ndipo mudzazindikira ndi kuona kuti choipa chanu munachichita pamaso pa Yehova ndi kudzipemphera mfumu, nchachikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi ino si nthawi yokolola tirigu? Komabe ndipemphera kwa Yehova kuti agwetse mvula ya mabingu. Zikatero mudzadziwa kuti tchimo lanu limene mwachita popempha mfumu kwa Yehova ndi lalikulu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Si nyengo yakumweta tirigu lero kodi? Ndidzaitana kwa Yehova, kuti atomize bingu ndi mvula; ndipo mudzazindikira ndi kuona kuti coipa canu munacicita pamaso pa Yehova ndi kudzipemphera mfumu, ncacikuru.