1 Samuel 12:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Samuele adatama Chauta mopemba, ndipo Chauta adatumizadi mvula yamabingu tsiku limenelo. Motero anthu onse adagwidwa ndi mantha aakulu oopa Chauta ndi Samuele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo Samuele anaitana kwa Yehova; ndipo Yehova anatumiza bingu ndi mvula tsiku lomwelo; ndipo anthu onse anaopa kwambiri Yehova ndi Samuele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Samueli anapemphera, ndipo Yehova anatumiza mvula ya mabingu tsiku lomwelo. Apo anthu aja anaopa kwambiri Yehova ndi Samueli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo Samueli anaitana kwa Yehova; ndipo Yehova anatumiza bingu ndi mvula tsiku lomwelo; ndipo anthu onse anaopa kwambiri Yehova ndi Samueli.