1 Samuel 12:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo anthu onse adauza Samuele kuti, “Chonde mutipempherere ife atumiki anu kwa Chauta, Mulungu wanu, kuti tingafe, pakuti pa machimo athu onse taonjezapo tchimo limeneli lopempha kuti tikhale ndi mfumu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu onse ananena ndi Samuele, Mupempherere akapolo anu kwa Yehova Mulungu wanu, kuti tingafe; popeza pamwamba pa zoipa zathu zonse tinaonjeza choipa ichi, chakuti tinadzipemphera mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anamupempha Samueli nati, “Chonde mutipempherere kwa Yehova, ife atumiki kuti tingafe pakuti pa machimo athu onse tawonjezapo tchimo lopempha mfumu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu onse ananena ndi Samueli, Mupempherere akapolo anu kwa Yehova Mulungu wanu, kuti tingafe; popeza pamwamba pa zoipa zathu zonse tinaonjeza coipa ici, cakuti tinadzipemphera mfumu.