1 Samuel 12:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano mfumu ndiyo izikutsogolerani. Ine nkukalamba kuno, kumutuku imvi zati mbuu, ndipo ana anga muli nawo pamodzi. Ndakhala ndikukutsogolerani kuyambira ndili mnyamata mpaka pano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, siyi mfumu idzayendabe pamaso panu; ndipo ine ndine wokalamba waimvi; ndipo, onani, ana anga amuna ali nanu, ndipo ine ndinayendabe pamaso panu kuyambira ubwana wanga kufikira lero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano muli ndi mfumu imene izikutsogolerani, koma ine ndakalamba, kumutu kwanga kuli imvi zokhazokha ndipo ana anga ali pamodzi ndi inu. Ndakhala ndili mtsogoleri wanu kuyambira ndili mnyamata mpaka lero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, siyi mfumu idzayendabe pamaso panu; ndipo ine ndine wokalamba waimvi; ndipo, onani, ana anga amuna ali nanu, ndipo ine ndinayendabe pamaso panu kuyambira ubwana wanga kufikira lero.