1 Samuel 12:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Samuele adaŵauza kuti, “Musaope. Kuchimwa mwachimwadi, komabe musaleke kutsata Chauta. Muzimtumikira ndi mtima wanu wonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Samuele ananena kwa anthuwo, Musaope; munachitadi choipa ichi chonse, koma musaleka kutsata Yehova, koma mutumikire Yehova ndi mtima wanu wonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Samueli anayankha kuti, “Musaope, inu mwachitadi tchimo ili, koma musaleke kumutsata Yehova ndi kumutumikira ndi mtima wanu wonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Samueli ananena kwa anthuwo, Musaope; munacitadi coipa ici conse, koma musaleka kutsata Yehova, koma mutumikire Yehova ndi mtima wanu wonse;