1 Samuel 12:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndili pompano, ngati chilipo chimene ndidalakwa, munditsutsiretu tsopano pamaso pa Chauta ndi pamaso pa wodzozedwa wake. Kodi ndani ndidamulandapo ng'ombe? Ndani ndidamulandapo bulu? Ndani ndidamdyererapo? Kodi ndani amene ndidamuzunza? Kodi nkwa yani ndidalandirapo chiphuphu choti nkundidetsa m'maso? Tsimikizeni, ndipo ndikubwezerani zonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndili pano. Ngati ndinalakwa chilichonse nditsutseni pamaso pa Yehova ndi wodzozedwa wake. Kodi ndinalanda ngʼombe ya yani? Kodi ndinalanda bulu wa yani? Kodi ndani amene ndinamudyera masuku pa mutu? Kodi ndinazunza yani? Kodi ndinalandira kwa yani chiphuphu choti nʼkundidetsa mʼmaso? Ngati ndinachita chilichonse cha izi, ine ndidzakubwezerani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndikalipo ine; citani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wace; ndinalanda ng'ombe ya yani? kapena ndinalanda buru wa yani? ndinanyenga yani? ndinasautsa yani? ndinalandira m'manja mwa yani cokometsera mlandu kutseka naco maso anga? ngati ndinatero ndidzacibwezera kwa inu.