1 Samuel 12:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yakobe ndi banja lake adapita ku dziko la Ejipito, Aejipito namaŵazunza, pamenepo makolo anuwo adadandaula kwa Chauta. Ndipo Chauta adatuma Mose ndi Aroni kuti aŵatulutse ku Ejipito ndi kudzaŵakhazika ku malo ano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Yakobo anafika ku Ejipito, ndi makolo anu anapemphera kwa Yehova, Yehova anatumiza Mose ndi Aroni, amene anatulutsa makolo anu m'Ejipito, nawakhalitsa pamalo pano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yakobo atapita ku dziko la Igupto, Aiguptowo akuwazunza, iwo analirira kwa Yehova kuti awathandize, ndipo Yehova anatumiza Mose ndi Aaroni, amene anatulutsa makolo anu mʼdziko la Igupto ndi kudzawakhazika pa malo ano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Yakobo anafika ku Aigupto, ndi makolo anu anapemphera kwa Yehova, Yehova anatumiza Mose ndi Aroni, amene anaturutsa makolo anu m'Aigupto, nawakhalitsa pamalo pano,