1 Samuel 12:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma makolo anuwo adaiŵala Chauta, Mulungu wao. Ndipo Mulungu adaŵapereka m'manja mwa Sisera, mtsogoleri wa ankhondo a mzinda wa Hazori. Adaŵaperekanso m'manja mwa Afilisti ndi m'manja mwa mfumu ya ku Mowabu. Adani onsewo adachita nkhondo ndi makolo anuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iwowa anaiwala Yehova Mulungu wao, Iye nawapereka m'dzanja la Sisera kazembe wa gulu la Hazori, ndi m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la mfumu ya Mowabu, iwo naponyana nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma iwo anayiwala Yehova Mulungu wawo, choncho Yehova anawapereka mʼdzanja la Sisera mkulu wa ankhondo wa mzinda wa Hazori, ndiponso mʼmanja mwa Afilisti ndi mfumu ya Mowabu. Mafumu onsewa anathira nkhondo makolo anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iwowa anaiwala Yehova Mulungu wao, iye nawapereka m'dzanja la Sisera kazembe wa gulu la Hazori, ndi m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la mfumu ya Moabu, iwo naponyana nao.