1 Samuel 13:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Samuele adamufunsa Sauloyo kuti, “Nanga nchiyaninso mwachitachi?” Iye adayankha kuti, “Pamene ndinaona kuti anthu akundithaŵira, ndipo kuti inuyo nthaŵi imene mudaanena ija simudabwere, ndiponso kuti Afilisti adasonkhana ku Mikimasi,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Samuele anati, Mwachitanji? Nati Saulo, Chifukwa ndinaona kuti anthuwo alinkubalalika kundisiya ine, ndi kuti inu simunafika masiku aja tinapangana, ndi kuti Afilisti anasonkhana ku Mikimasi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Samueli anafunsa kuti, “Nʼchiyani chimene wachita?” Sauli anayankha kuti, “Nditaona kuti anthu ayamba kundithawa, ndi kuti inu simunabwere pa nthawi munanena ija, ndiponso kuti Afilisti akusonkhana ku Mikimasi,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Samueli anati, Mwacitanji? Nati Sauli, Cifukwa ndinaona kuti anthuwo alinkubalalika kundisiya ine, ndi kuti inu simunafika masiku aja tinapangana, ndi kuti Afilisti anasonkhana ku Mikimasi;