1 Samuel 13:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndinati, ‘Tsopano Afilisti abwera kudzandithira nkhondo ku Giligala kuno, ine ndisanapemphe Chauta kuti andikomere mtima.’ Motero ndinadzikakamiza kupereka nsembe yopserezayi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake ndinati, Afilisti adzatitsikira pano pa Giligala, ndisanapembedze Yehova; potero ndinadzifulumira, ndi kupereka nsembe yopsereza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndinati, ‘Tsopano Afilisti abwera kudzandithira nkhondo ku Giligala kuno, chonsecho sindinapemphe Yehova kuti andikomere mtima.’ Motero ndinakakamizika kupereka nsembe yopsereza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace ndinati, Afilisti adzatitsikira pane pa Giligala, ndisanapembedze Yehova; potero ndinadzifulumiza, ndi kupereka nsembe yopsereza.