1 Samuel 13:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyi nkuti mulibe msuli ndi mmodzi yemwe m'dziko lonse la Israele, chifukwa Afilisti ankati, “Tisaŵalole Ahebri kuti azidzisulira okha malupanga ndi mikondo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'dziko lonse la Israele simunapezeka wosula; popeza Afilisti adati, Kuti Aisraele angadzisulire malupanga kapena mikondo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyo nʼkuti mulibe osula zitsulo mʼdziko lonse la Israeli, pakuti Afilisti anati, “Tisawalole Aheberi kudzipangira okha malupanga kapena mikondo!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'dziko lonse la Israyeli simunapezeka wosula; popeza Afilisti adati, Kuti Aisrayeli angadzisulire malupanga kapena mikondo;