1 Samuel 13:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ina iye adasankha Aisraele 3,000. Mwa ameneŵa, 2,000 anali ndi Sauloyo ku Mikimasi ndi ku dziko lamapiri ku Betele, ndipo 1,000 anali ndi Yonatani ku Gibea m'dziko la Benjamini. Anthu ena onse otsala adaŵabweza kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi ina Sauli anasankha Aisraeli 3,000. Mwa iwowa, 2,000 anali ndi Sauliyo ku Mikimasi ndi ku dziko la mapiri ku Beteli, ndipo 1,000 anali ndi Yonatani ku Gibeya ku Benjamini. Anthu ena onse otsala anawabweza kwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Sauli anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israyeli; zikwi ziwiri za iwowa zinali ndi Sauli ku Mikimasi, ndi ku phiri la ku Beteli; ndi cikwi cimodzi anali ndi Jonatani ku Gibeya wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.