1 Samuel 13:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Mwisraele aliyense ankapita kwa Afilisti kukasanjitsa pulao kapena khasu lake, ndi kukanoletsa nkhwangwa yake kapena chikwakwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma Aisraele onse ankatsikira kwa Afilisti, kuti awasanjire munthu yense chikhasu chake, cholimira chake, nkhwangwa yake, ndi chisenga chake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero Aisraeli onse amapita kwa Afilisti kukanoletsa mapulawo, makasu, nkhwangwa ndi zikwakwa zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma Aisrayeli onse adafotsikira kwa Afilisti, kuti awasaniire munthu yense cikhasu cace, colimira cace, nkhwangwa yace, ndi khasu lace;