1 Samuel 13:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero tsiku lankhondolo panalibe lupanga kapena mkondo m'manja mwa Mwisraele aliyense amene ankatsata Saulo ndi Yonatani. Koma Saulo ndi mwana wake Yonatani, iwo okha ndiwo anali nazo zida.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho kunali kuti tsiku lankhondolo sunapezeka mkondo kapena lupanga m'manja a anthu onse anali ndi Saulo ndi Yonatani; koma Saulo yekha ndi Yonatani mwana wake anali nazo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero tsiku la nkhondolo panalibe lupanga kapena mkondo mʼdzanja la aliyense amene anatsatira Saulo ndi Yonatani. Koma Saulo ndi Yonatani, iwo okha ndiwo anali ndi zida.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco kunali kuti tsiku lankhondolo sunapezeka mkondo kapena lupanga m'manja a anthu onse anali ndi Sauli ndi Jonatani; koma Sauli yekha ndi Jonatani mwana wace anali nazo.