1 Samuel 13:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yonatani adapha mkulu wa ankhondo wachifilisti amene anali ku Geba, ndipo Afilisti adamva zimenezi. Apo Saulo adatuma amithenga kuti alize lipenga lankhondo m'dziko lonselo, nanena kuti, “Ahebri amve.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yonatani anathyola kaboma ka Afilisti lokhala ku Geba, ndipo Afilisti anamva za ichi. Ndipo Saulo analiza lipenga m'dziko monse, nati, Amve Ahebri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yonatani anakantha mkulu wa ankhondo wa Afilisti ku Geba, ndipo Afilisti anamva kuti Aheberi awukira. Tsono Sauli anawuza amithenga kuti alize lipenga mʼdziko lonse la Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Jonatani anathyola kaboma ka Afilisti lokhala ku Geba, ndipo Afilisti anamva za ici. Ndipo Sauli analiza lipenga m'dziko monse, nati, Amve Ahebri.