1 Samuel 13:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Aisraele onse adamva mbiri yakuti Saulo adapha mkulu wa ankhondo wachifilisti, ndiponso kuti Afilisti anali ataipidwa kwambiri ndi Aisraele. Motero anthu adaitanidwa kuti abwere kwa Saulo ku Giligala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aisraele onse anamva kunena kuti Saulo anathyola kaboma ka Afilisti, ndi kuti Afilisti anyansidwa ndi Aisraele. Ndipo anthuwo anasonkhana kwa Saulo ku Giligala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Aisraeli onse anamva kuti Sauli wakantha mkulu wa ankhondo Wachifilisiti ndi kuti Afilisti anayipidwa nawo Aisraeli. Ndiye anthu anayitanidwa kuti abwere kwa Sauli ku Giligala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Aisrayeli onse anamva kunena kuti Sauli anathyola kaboma ka Afilisti, ndi kuti Afilisti anyansidwa ndi Aisrayeli. Ndipo anthuwo anasonkhana kwa Sauli ku Giligala.