1 Samuel 13:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Afilisti adasonkhana pamodzi kuti amenyane nkhondo ndi Aisraele. Adasonkhanitsa magaleta ankhondo 30,000, okwera pa akavalo 6,000 ndi ankhondo ochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Iwowo adapita nakamanga zithando zao ku Mikimasi, kuvuma kwa Betaveni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisraele, anali nao magaleta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi anthu akuchuluka monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum'mawa kwa Betaveni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Afilisti anasonkhana kuti amenyane ndi Aisraeli. Iwo anali ndi magaleta 3,000, okwera pa akavalo 2,000 ndiponso asilikali kuchuluka kwake ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Iwo anapita ndi kukamanga misasa yawo ku Mikimasi, kummawa kwa Beti-Aveni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisrayeli, anali nao magareta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi cimodzi, ndi anthu akucuruka monga mcenga wa pa dooko la nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum'mawa kwa Betaveni.