1 Samuel 13:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Aisraele adaona kuti ali m'zoopsa, poti anali atapanikizidwadi kwambiri, adakabisala m'mapanga, m'maenje, m'matanthwe, m'makwaŵa ndi m'zitsime.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene anthu a Israele anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Aisraeli anaona kuti anali pamavuto akulu, poti anali atapanikizidwa kwambiri, anabisala mʼmapanga, mʼmaenje, mʼmatanthwe, mʼmakwalala ndi mʼzitsime.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene anthu a Israyeli anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje.