1 Samuel 13:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ena adaoloka Yordani mpaka kukafika ku dziko la Gadi ndi ku Giliyadi. Saulo anali ku Giligalabe, ndipo anthu okhala naye anali njenjenje ndi mantha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ahebri ena anaoloka Yordani nafika ku dziko la Gadi ndi Giliyadi; koma Saulo akali ku Giligala, ndipo anthu onse anamtsata ndi kunthunthumira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahebri ena anawoloka Yorodani mpaka kukafika ku dziko la Gadi ndi ku Giliyadi. Koma Sauli anakhalabe ku Giligala ndipo ankhondo onse amene anali naye anali njenjenje ndi mantha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ahebri ena anaoloka Yordano nafika ku dziko la Gadi ndi Gileadi; koma Sauli akali ku Giligala, ndipo anthu onse anamtsata ndi kunthunthumira.