1 Samuel 14:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Yonatani, mwana wa Saulo, adauza mnyamata womnyamulira zida zake zankhondo kuti, “Tiye tiwolokere tipite ku kaboma kankhondo ka Afilisti tsidya ilo.” Koma sadauze bambo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali tsiku lina kuti Yonatani mwana wa Saulo ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite kunka ku kaboma ka Afilisti, tsidya lija. Koma sanauze atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina Yonatani mwana wa Sauli anawuza mnyamata wake womunyamulira zida zake za nkhondo kuti, “Tiye tiwoloke tipite ku kaboma ka Afilisti tsidya ilo.” Koma iye sanawuze abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali tsiku lina kuti Jonatani mwana wa Sauli ananena ndi mnyamata wonyamula zida zace, Tiye tipite kunka ku kaboma ka Afilisti, tsidya lija. Koma sanauza atate wace.