1 Samuel 14:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho aŵiriwo adadziwonetsa ku kaboma kankhondo ka Afilisti. Tsono Afilisti adati, “Taonani Ahebri akutuluka m'maenje m'mene ankabisala.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo onse awiri anadziwulula kwa a ku kaboma ka Afilistiwo; ndipo Afilistiwo anati, Onani, Ahebri alikutuluka m'mauna m'mene anabisala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho awiriwa anadzionetsa ku kaboma ka nkhondo ka Afilisti. Tsono Afilistiwo anati, “Taonani! Aheberi akutuluka mʼmaenje mʼmene anabisala.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo onse awiri anadziulula kwa a ku kaboma ka Afilistiwo; ndipo Afilistiwo anati, Onani, Ahebri alikuturuka m'mauna m'mene anabisala.