1 Samuel 14:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo anthu akukabomawo adafuulira Yonatani ndi mnyamata wake uja kuti, “Tabwerani kuno, muwona!” Apo Yonatani adauza mnyamata wakeyo kuti, “Unditsate, Chauta wapereka anthuŵa m'manja mwa Aisraele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo a ku kabomawo anayankha Yonatani ndi wonyamula zida zake, nati, Kwerani kuno kwa ife, tikuonetseni kanthu. Ndipo Yonatani, anauza wonyamula zida zake, Kwera unditsate m'mbuyo, pakuti Yehova wawapereka m'dzanja la Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku kaboma kaja anafuwula kwa Yonatani ndi mnyamata wake uja kuti, “Bwerani kuno ndipo tikuphunzitsani phunziro.” Ndipo Yonatani anati kwa mnyamata wake. “Nditsate pakuti Yehova wapereka Afilistiwa mʼmanja mwa Aisraeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo a ku kabomawo anayankha Jonatani ndi wonyamula zida zace, nati, Kwerani kuno kwa ife, tikuonetseni kanthu. Ndipo Jonatani anauza wonyamula zida zace, Kwera unditsate m'mbuyo, pakuti Yehova wawapereka m'dzanja la Israyeli.