1 Samuel 14:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Yonatani adakwera chokwaŵa, mnyamata wake uja akumtsata pambuyo. Tsono Yonatani adaŵathira nkhondo Afilistiwo ndi kumaŵagwetsa, mnyamata wake uja nkumaŵapha pambuyo pa iyeyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yonatani anakwera chokwawa, ndi wonyamula zida zake anamtsata; ndi Afilisti anagwa pamaso pa Yonatani, ndi wonyamula zida zake anawapha pambuyo pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yonatani anakwera mokwawa, ndipo mnyamata wake uja ankamutsata. Tsono Yonatani anathira nkhondo Afilisti aja namawagwetsa, ndipo mnyamata wake uja ankawapha pambuyo pa iyeyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Jonatani anakwera cokwawa, ndi wonyamula zida zace anamtsata; ndi Afilisti anagwa pamaso pa Jonatani, ndi wonyamula zida zace anawapha pambuyo pace.