1 Samuel 14:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Afilisti onse m'dzikomo adasokonezeka ndi mantha aakulu. Ankhondo a ku kaboma kankhondo kaja ndi anzao enanso ankanjenjemera kwambiri. Kudachita chivomezi ndipo kugwedezeka kwa dziko kudakulitsa mantha a Afilisti aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono gulu lonse la ankhondo, ndiye kuti iwo amene anali mʼmisasa ndi mʼminda ndiponso iwo amene anali ku kaboma ka ankhondo kaja, onse anagwidwa ndi mantha aakulu. Dzikonso linagwedezeka, choncho anthu anachita mantha koopsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; comweco kunali kunthunthumira kwakukuru koposa,