1 Samuel 14:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Saulo ankalankhula ndi wansembeyo, phokoso linkakulirakulira ku zithando za Afilisti. Tsono Saulo adauza wansembe uja kuti, “Leka, usaombeze!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali m'mene Saulo anali chilankhulire ndi wansembeyo, phokoso la m'chigono cha Afilisti linachitikabe, nilikula; ndipo Saulo ananena ndi wansembeyo, Bweza dzanja lako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Sauli amayankhula ndi wansembe, phokoso limanka likulirakulira mu msasa wa Afilisti, Kotero Sauli anati kwa wansembe, “Leka kuwombeza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali m'mene Sauli anali cilankhulire ndi wansembeyo, phokoso la m'cigono ca Afilisti linacitikabe, nilikula; ndipo Sauli ananena ndi wansembeyo, Bweza dzanja lako.