1 Samuel 14:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Saulo pamodzi ndi anthu amene anali naye adasonkhananso napita kukamenya nkhondo, ndipo adaona Afilisti akungophana okhaokha. Motero kunali chisokonezo chachikulu kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo ndi anthu onse amene anali naye anaunjikana pamodzi, natulukira kunkhondoko; ndipo taonani, munthu yense anakantha mnzake ndi lupanga, ndipo panali kusokonezeka kwakukulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Sauli ndi asilikali onse amene anali naye anasonkhana kupita kukamenya nkhondo, ndipo anangoona chisokonezo chachikulu kwambiri. Afilisti akuphana okhaokha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli ndi anthu onse amene anali naye anaunjikana pamodzi, naturukira kunkhondoko; ndipo taonani, munthu yense anakantha mnzace ndi lupanga, ndipo panali kusokonezeka kwakukuru.