1 Samuel 14:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ataloŵa m'nkhalangomo, adangoona uchi ukukha pansi, koma panalibe amene adatengako kuika pakamwa, poti ankaopa temberero lija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakufika anthuwo m'nkhalangomo, onani, madzi a uchi anachuluka; koma panalibe munthu mmodzi anaika dzanja lake pakamwa, pakuti anthuwo anaopa tembererolo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atalowa mʼnkhalango, anaona uchi ukukha, koma palibe amene anadya, pakuti ankaopa lumbiro lija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakufika anthuwo m'nkhalangomo, onani, madzi a uci anacuruka; koma panalibe munthu mmodzi anaika dzanja lace pakamwa, pakuti anthuwo anaopa tembererolo.