1 Samuel 14:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yonatani anali asanamve za temberero la bambo wake lija. Choncho adatosa chisa cha njuchi ndi nsonga ya ndodo imene inali m'manja mwake, naika uchi wake pakamwa naadya. Atatero m'maso mwake mudachita kuti ngwee.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yonatani sanamve m'mene atate wake analumbirira anthu; chifukwa chake iye anatambalitsa ndodo ya m'dzanja lake, naitosa m'chisa cha uchi, naika dzanja lake pakamwa pake; ndipo m'maso mwake munayera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yonatani sanamve kuti abambo ake anawalumbirira anthu aja choncho anatenga ndodo yake imene inali mʼdzanja lake ndipo anayipisa mu chisa cha njuchi. Choncho iye anadya uchiwo ndipo mʼmaso mwake munayera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Jonatani sanamva m'mene atate wace analumbirira anthu; cifukwa cace iye ana tam balitsa ndodo ya m'dzanja lace, naitosa m'cisa ca uci, naika dzanja lace pakamwa pace; ndipo m'maso mwace munayera.