1 Samuel 14:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mmodzi mwa anthuwo adati, “Bambo wanu waopseza anthu pakunena kuti, ‘Atembereredwe amene adye kanthu lero.’ Nchifukwa chake anthuŵa akuchita ngati akomoke ndi njala.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wina wa anthuwo anayankha, nati, Atate wanu analangiza anthu kolimba ndi lumbiro, ndi kuti, Wotembereredwa iye wakudya lero chakudya. Ndipo anthuwo analema.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mmodzi mwa Asilikali anamuwuza kuti, “Abambo ako alumbirira anthu nati, ‘Wotembereredwa munthu aliyense amene adye chakudya lero.’ Nʼchifukwa chake anthu alefuka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wina wa anthuwo anayankha, nati, Atate wanu analangiza anthu kolimba ndi lumbiro, ndi kuti, Wotembereredwa iye wakudya lero cakudya. Ndipo anthuwo analema.