1 Samuel 14:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panalinso Ahiya, wansembe amene ankavala efodi. Iyeyo anali mwana wa Ahitubi, mbale wa Ikabodi mwana wa Finehasi. Finehasiyo anali mwana wa Eli, wansembe wa Chauta ku Silo. Tsono anthu sankadziŵa kuti Yonatani wachokapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wake wa Ikabodi, mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wovala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwe kuti Yonatani wachoka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakati pawo panalinso Ahiya amene ankavala efodi. Iye anali mwana wa Ahitubi, mʼbale wake wa Ikabodi mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo. Koma palibe amene anadziwa kuti Yonatani wachoka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wace wa Ikabodi, mwana wa Pinehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wobvala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwa kuti Jonatani wacoka.