1 Samuel 14:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kukadakhala bwino kwambiri, anthu akadadya mwaufulu lero zofunkha zimene adazipeza kwa adani ao. Zidakatero bwenzi tsopano lino titapha Afilisti ambiri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koposa kotani nanga, ngati anthu akadadya nakhuta zowawanya anazipeza za adani ao? Popeza tsopano palibe kuwapha kwakukulu kwa Afilisti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zikanakhala zabwino kwambiri anthuwa akanadya lero zofunkha za adani awo. Zikanatero tikanapha Afilisti ochuluka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koposa kotani nanga, ngati anthu akadadya nakhuta zowawanya anazipeza za adani ao? popeza tsopano palibe kuwapha kwakukuru kwa Afilisti.