1 Samuel 14:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adatinso, “Mwazikanani pakati pa anthu, muŵauze kuti, ‘Aliyense abwere ndi ng'ombe yake, kapena nkhosa yake, aziphere pompano, kenaka adye. Ndipo musachimwire Chauta podyera kumodzi ndi magazi.’ ” Motero aliyense mwa anthuwo adabwera ndi ng'ombe yake usiku umenewo, naiphera komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo anati, Balalikani pakati pa anthu, nimuwauze kuti abwere kwa ine kuno munthu yense ndi ng'ombe yake, ndi munthu yense ndi nkhosa yake, aziphe pano, ndi kuzidya, osachimwira Yehova ndi kudya zamwazi. Nabwera anthu onse, yense ndi ng'ombe yake, usiku uja naziphera pomwepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Sauli anati, “Mwazikanani pakati pa anthu ndi kukawawuza kuti aliyense abwere ndi ngʼombe yake kapena nkhosa yake, ndipo adzayiphe pomwe pano ndi kuyidya. Musachimwire Yehova pakudya nyama imene ili ndi magazi.” Kotero aliyense anabwera ndi ngʼombe yake usiku womwewo ndi kuyipha pomwepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli anati, Balalikani pakati pa anthu, nimuwauze kuti abwere kwa ine kuno munthu yense ndi ng'ombe yace, ndi munthu yense ndi nkhosa yace, aziphe pano, ndi kuzidya, osacimwira Yehova ndi kudya zamwazi. Nabwera anthu onse, yense ndi ng'ombe yace, usiku uja naziphera pomwepo.