1 Samuel 14:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Saulo adati, “Tiyeni tipite usiku, tilondole Afilisti, ndipo tilande zinthu zao mpaka m'maŵa kutacha. Tisasiyepo ndi mmodzi yemwe mwa iwo.” Anthuwo adati, “Chitani chilichonse chimene chikukukomerani.” Koma wansembe adati, “Tiyeni tiyambe tapempha nzeru kwa Mulungu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo anati, Tiyeni titsikire usiku kwa Afilistiwo, ndi kuwawawanya kufikira kutayera, tisasiye munthu mmodzi wa iwowa. Ndipo iwo anati, Chitani chilichonse chikukomerani. Pamenepo wansembeyo anati, Tisendere kwa Yehova kuno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli anati, “Tiyeni titsatire Afilisti usikuwu ndi kulanda zinthu zawo mpaka mmawa. Tisasiyepo wamoyo ndi mmodzi yemwe.” Ankhondowo anayankha kuti, “Chitani chilichonse chimene chikukomerani.” Koma wansembe anati, “Tipemphe uphungu kwa Mulungu poyamba.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli anati, Tiyeni titsikire usiku kwa Afilistiwo, ndi kuwawawanya kufikira kutayera, tisasiye munthu mmodzi wa iwowa. Ndipo iwo anati, Citani ciri conse cikukomerani. Pamenepo wansembeyo anati, Tisendere kwa Yehova kuno.