1 Samuel 14:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pali Chauta, Mpulumutsi wa Aisraele, wochimwayo ngakhale akhale mwana wanga Yonatani, afe ndithu.” Koma panalibe ndi mmodzi yemwe pakati pa anthu onsewo amene adamuyankha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israele, chingakhale chili m'mwana wanga Yonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pali Yehova amene amapulumutsa Israeli, ngakhale tchimolo litapezeka ndi mwana wanga Yonatani, iye afe ndithu.” Koma palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthuwo amene anamuyankha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israyeli, cingakhale ciri m'mwana wanga Jonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye.