1 Samuel 14:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pampata pamene Yonatani ankafuna kudzerapo kuti akafike ku kaboma kankhondo kaja, panali thanthwe lotsetsereka mbali ina, ndi lina lotsetsereka mbali inanso. Dzina la thanthwe lina ankati Bozezi, ndipo linalo ankati Sene.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakati pa mipata imene Yonatani anafuna kupitapo kunka ku kaboma ka Afilisti, panali phiri lathanthwe pa mbali ina, ndi phiri lathanthwe pa mbali inzake; ndipo dzina la linalo ndilo Bozezi, ndi la linzake ndilo Sene.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa mpata pamene Yonatani ankafuna kudutsa kukafika ku kaboma ka nkhondo ka Afilisti kunali thanthwe lotsetsereka mbali ina ndi lina lotsetsereka mbali inayo. Thanthwe limodzi linkatchedwa Bozezi ndipo linalo linkatchedwa Seni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakati pa mipata imene Jonatani anafuna kupitapo kunka ku kaboma ka Afilisti, panali phiri lathanthwe pa mbali yina, ndi phiri lathanthwe pa mbali inzace; ndipo dzina la linalo ndilo Bozezi, ndi la linzace ndilo Sene.