1 Samuel 14:40 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adauza Aisraelewo kuti, “Inu mukhale mbali imodzi, ine ndi mwana wanga Yonatani tikhalanso mbali ina.” Anthuwo adauza Saulo kuti, “Muchite zimene zikukomereni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye ananena ndi Aisraele onse, Inu mukhale mbali ina, ndipo ine ndi Yonatani mwana wanga tidzakhala mbali yinanso. Ndipo anthuwo ananena ndi Saulo, Chitani chimene chikukomerani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Sauli anawuza Aisraeli onse kuti, “Inu mukhale mbali imodzi. Ine ndi mwana wanga Yonatani tikhala mbali inayo.” “Chitani chilichonse chimene chikukomerani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye ananena ndi Aisrayeli onse, Inu mukhale mbali yina, ndipo me ndi Jonatani mwana wanga tidzakhala mbali yinanso. Ndipo anthuwo ananena ndi Sauli, Citani cimene cikukomerani.