1 Samuel 14:41 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Saulo adati, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, chifukwa chiyani simudandiyankhe ine mtumiki wanu lero lino? Ngati wolakwa ndineyo kapena mwana wanga Yonatani, Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, aoneke ndi Urimu. Koma tchimolo likakhala la Aisraele, aoneke ndi Tumimu.” Maere adagwera Yonatani ndi Saulo, anthu nkupulumuka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Saulo ananena ndi Yehova, Mulungu wa Israele, muonetse choonadi. Ndipo maere anagwera Saulo ndi Yonatani; koma anthuwo anapulumuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Sauli anapemphera kwa Yehova Mulungu wa Israeli kuti, “Chifukwa chiyani simunandiyankhe ine mtumiki wanu lero lino? Ngati tchimoli lipezeka ndi ine kapena ndi Yonatani mwana wanga, Inu Mulungu wa Israeli, aoneke ndi Urimu. Koma ngati wochimwa ndi anthu anu, Aisraeli aoneke Tamimu.” Maere anagwera Sauli ndi Yonatani ndipo anthu anapezeka osalakwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Sauli ananena ndi Yehova, Mulungu wa Israyeli, muonetse coonadi. Ndipo maere anagwera Sauli ndi Jonatani; koma anthuwo anapulumuka.