1 Samuel 14:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Saulo adauza Yonatani kuti, “Tandiwuza zimene wachita.” Yonatani adauza bambo wakeyo kuti, “Ndidalaŵako uchi pang'ono ndi nsonga ya ndodo yanga. Ndiye ai, chomwecho, ine ndili wokonzeka kuti ndife.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Saulo ananena ndi Yonatani, Undiuze chimene unachita. Ndipo Yonatani anamuuza, nati, Zoonadi ndinangolawako uchi pang'ono ndi nsonga ya ndodo inali m'dzanja langa: ndipo onani ndiyenera kufa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Sauli anati kwa Yonatani, “Ndiwuze chimene wachita.” Ndipo Yonatani anamuwuza kuti, “Ine ndinangolawa uchi pangʼono ndi ndodo yangayi. Ndiye ine ndili wokonzeka kufa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Sauli ananena ndi Jonatani, Undiuze cimene unacita. Ndipo Jonatani anamuuza, nati, Zoonadi ndinangolawako uci pang'ono ndi nsonga ya ndodo inali m'dzanja langa: ndipo onani ndiyenera kufa.