1 Samuel 14:45 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu adafunsa Saulo kuti, “Kodi afe Yonatani amene wagwira ntchito yopulumutsa Aisraele kunkhondo? Sizingatheke mpang'ono pomwe. Pali Chauta wamoyo! Tsitsi nlimodzi lomwe la kumutu kwake silipezeka lothothoka. Zimene wachita lerozi, wamthandiza ndi Mulungu.” Motero anthu adamupulumutsa Yonatani, ndipo sadaphedwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthuwo ananena ndi Saulo, kodi Yonatani adzafa, amene anachititsa chipulumutso chachikulu ichi m'Israele? Musatero. Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la pa mutu wake lidzagwa pansi, pakuti iye anagwirizana ndi Mulungu lero. Chomwecho anthuwo anapulumutsa Yonatani kuti angafe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthuwo anafunsa Saulo kuti, “Kodi Yonatani afe, iye amene wagwira ntchito iyi yayikulu yopulumutsa Aisraeli? Osatheka! Pali Yehova ngakhale tsitsi ndi limodzi lomwe lapamutu pake silidzathothoka, pakuti wachita zimenezi lero ndi thandizo la Mulungu.” Choncho anthuwo anamupulumutsa Yonatani, ndipo sanaphedwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthuwo ananena ndi Sauli, Kodi Jonatani adzafa, amene anacititsa cipulumutso cacikuru ici m'Israyeli? Musatero. Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la pa mutu wace lidzagwa pansi, pakuti iye anagwirizana ndi Mulungu lero. Comweco anthuwo anapulumutsa Jonatani kuti angafe. Ndipo Sauli analeka kuwapitikitsa Afilistiwo;