1 Samuel 14:48 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adachita zamphamvu, ndipo adagonjetsa Aamaleke. Motero adapulumutsa Aisraele kwa anthu amene ankaŵalanda zinthu zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anakula mphamvu, nakantha Aamaleke, napulumutsa Aisraele m'manja a akuwawawanya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anachita nkhondo mwamphamvu ndi kugonjetsa Aamaleki. Choncho anapulumutsa Aisraeli mʼmanja mwa anthu amene ankawalanda zinthu zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anakula mphamvu, nakantha Aamaleki, napulumutsa Aisrayeli m'manja a akuwawawanya.