1 Samuel 14:50 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkazi wa Saulo anali Ahinowamu mwana wa Ahimaazi. Ndipo mkulu wa ankhondo a Saulo anali Abinere, mwana wa Nere, mbale wa bambo wa Saulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi dzina la mkazi wa Saulo ndi Ahinowamu mwana wa Ahimaazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lake ndiye Abinere mwana wa Nere, mbale wake wa atate wa Saulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzina la mkazi wake linali Ahinoamu. Iyeyu anali mwana wa Ahimaazi. Dzina la mkulu wa ankhondo a Sauli linali Abineri mwana wa Neri, mʼbale wa abambo a Sauli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi dzina la mkazi wa Sauli ndi Ahinamu mwana wa Ahimazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lace ndiye Abineri mwana wa Neri, mbale wace wa atate wa Sauli.