1 Samuel 14:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yonatani adauza mnyamata wake uja kuti, “Tiye tiwolokere tipite ku kaboma kankhondo ka anthu osaumbalidwaŵa. Mwina mwake Chauta atigwirira ntchito. Pakuti palibe chomletsa Chauta kutipambanitsa ngakhale tikhale ochepa chotani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chomletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yonatani anawuza mnyamata wake womunyamulira zida uja kuti, “Tiye tiwoloke tipite ku kaboma ka anthu osachita mdulidwewo. Mwina Yehova adzatigwirira ntchito. Palibe chomuletsa Yehova kutipulumutsa, ngakhale tikhale ambiri kapena ochepa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Jonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zace, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira nchito; pakuti palibe comletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.