1 Samuel 14:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mnyamata wakeyo adati, “Muchite zonse monga momwe mtima wanu ufunira. Ine ndili nanu, ndipo monga momwe mukuganizira inu, ine mmomwemonso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wonyamula zida zake anena naye, Chitani zonse zili mumtima mwanu; palukani, onani ndili pamodzi ndi inu monga mwa mtima wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mnyamata uja anati, “Chitani chilichonse chimene mtima wanu ukhumba. Ine ndili nanu pamodzi. Chimene mtima wanu ukhumba ndi chomwenso ine ndikhumba.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wonyamula zida zace ananena naye, Citani zonse ziri mumtima mwanu; palukani, onani ndiri pamodzi ndi inu monga mwa mtima wanu.