1 Samuel 15:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'mamaŵa ndithu, Samuele adadzuka kuti akakumane ndi Saulo. Anthu adamuuza kuti, “Saulo adabwera ku Karimele, ndipo kumeneko adadziimikira mwala wa chikumbutso cha iye mwini. Tsono adachokapo napitirira mpaka ku Giligala.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Samuele analawirira m'mawa kuti akakomane ndi Saulo; ndipo munthu anamuuza Samuele kuti, Saulo anafika ku Karimele, ndipo taonani, anaimika chikumbutso chake, nazungulira, napitirira, natsikira ku Giligala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Samueli anadzuka mmamawa ndipo anapita kukakumana ndi Sauli. Koma anthu anamuwuza kuti, “Sauli anabwera ku Karimeli, ndipo kumeneko wadziyimikira mwala wachikumbutso cha iye mwini. Tsopano wachokako ndipo wapita ku Giligala.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Samueli analawirira m'mawa kuti akakomane ndi Sauli; ndipo munthu anamuuza Samueli kuti, Sauli anafika ku Karimeli, ndipo taonani, anaimika cikumbutso cace, nazungulira, napitirira, natsikira ku Giligala.