1 Samuel 15:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Samuele adamuuza kuti, “Basi, musapitirize! Imani ndikukambireni zimene Chauta wandiwuza usiku.” Tsono Saulo adati, “Nenani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo Samuele ananena ndi Saulo, Imani, ndidzakudziwitsani chimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Samueli anati kwa Sauli, “Khala chete! Ima ndikuwuze zimene Yehova wandiwuza usiku wathawu.” Sauli anayankha kuti, “Ndiwuzeni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo Samueli ananena ndi Sauli, Imani, ndidzakudziwitsani cimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani.