1 Samuel 15:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Samuele adati, “Ngakhale kale munali wamng'ono pamaso pa anthu, tsopano mwasanduka mtsogoleri wa mafuko onse a Aisraele. Chauta adakudzozani kuti mukhale mfumu yomalamulira Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Samuele, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwa mutu wa mafuko a Israele? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Apo Samueli anati, “Munali wamngʼono pa maso pa anthu, koma tsopano mwasanduka mtsogoleri wa mafuko a Israeli. Yehova anakudzozani kuti mukhale mfumu yolamulira Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Samueli, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwa mutu wa mafuko a Israyeli? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israyeli,