1 Samuel 15:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Ndidzalanga Aamaleke chifukwa cha kumenyana ndi Aisraele pa njira, pamene Aisraelewo ankachokera ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova wa makamu, Ndinaonerera chimene Amaleke anachitira Israele, umo anamlalira panjira, m'mene iye anakwera kutuluka m'Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndidzalanga Aamaleki chifukwa cha zimene anawachita Aisraeli. Paja iwo analimbana ndi Aisraeli pa njira pamene Aisraeliwo ankachoka ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova wa makamu, Ndinaonerera cimene Amaleki anacitira Israyeli, umo anamlalira panjira, m'mene iye anakwera kuturuka m'Aigupto.